Tonse tikuitanidwa ndi Mulungu kulingalira pamodzi ndi Iye. Mkhalidwe uwu wa Mulungu pa munthu ndi chionetsero cha Chikondi chake. Mulungu watipatsa Mawu ake, Baibulo, mmene timapeza mayankho a mafunso ofunika kwambiri pa moyo. Chotero, tiyeni titembenukire ku Bukhu Lodabwitsali kuti tipeze mayankho a mafunso ofunika kwambiri amene ambiri a ife, panthaŵi ina kapena inzake, takhala tikulingalirapo. Malemba ogwidwa mawu apa anasankhidwa ndi kulingalira koyenera ku nkhani yonse imene ili njira yokha yowona mtima yopezera mayankho olondola a m’Malemba. Mafunso amene ali m’masamba otsatirawa ali m’gulu la mafunso ofunika kwambiri amene amadziwonetsera okha m’maganizo mwathu ndipo amayankhidwa mokwanira m’Baibulo. Izi ndi zitsanzo chabe za Malemba ena ambiri amene angaperekedwe. Yesu anati: “Ngati mukhala m’mawu anga, muli akuphunzira anga ndithu; mudzazindikira chowonadi, ndipo chowonadi chidzakumasulani.”—Yohane 8:31-32
“Chomwe mu nthawi Zake Iye adzasonyeza amene ali Wodala ndi Wamphamvu yekhayo, Mfumu ya Mafumu, ndi Mbuye wa ambuye, amene ali ndi moyo wosakhoza kufa, wokhala m’Kuwala kumene palibe munthu angayandikireko, amene palibe munthu anamuonapo, kapena angathe. onani!” 1 Timoteyo 6:15, 16
“Moyo wochimwawo ndiwo udzafa. Ezekieli 18:20
“Musamaopa amene akupha thupi, koma moyo sangathe kuupha; koma makamaka muope Iye, wokhoza kuononga moyo ndi thupi lomwe m’Gehena. Mateyu 10:28
“M’thukuta la nkhope yako udzadya chakudya, kufikira kuti udzabwerera kunthaka: chifukwa kuti mmenemo unatengedwa: ndiwe fumbi, ndi kufumbiko udzabwerera. (Kunena za imfa ya thupi.) Genesis 3:19
“Koma sindifuna kuti mukhale osadziwa, abale, za iwo akugona (akufa) kuti musalire, monganso ena amene alibe chiyembekezo.” 1 Atesalonika 4:13
“Mpweya wake uchoka, abwerera kumka ku nthaka yake; tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake zitayika. Salmo 146:4
"...palibe munthu anakwera Kumwamba, koma Iye wotsikayo kuchokera Kumwamba, ndiye Mwana wa munthu." (Onse adakali m’manda mpaka kuuka kwa akufa.) Yohane 3:13
“…ngati akufa saukitsidwa, Kristunso sanaukitsidwa; ndipo ngati Khristu sanaukitsidwa, chikhulupiriro chanu chiri chopanda pake; mukali m’machimo anu. Pamenepo iwo akugona mwa Khristu atayika. 1 Akorinto 15:15-18
“Pakuti Ambuye adzatsika Kumwamba mwini yekha ndi mfuu, ndi mawu a Mngelo wamkulu, ndi lipenga la Mulungu; ndipo akufa mwa Khristu adzayamba kuuka.” 1 Atesalonika 4:16
“Pakuti monga mwa Adamu onse amwalira, koteronso mwa Khristu onse akhalitsidwa ndi moyo.” 1 Akorinto 15:21, 22
“…ikudza nthawi imene onse ali m’manda adzamva mawu ake, nadzatulukira. Yohane 5:28, 29
“Chifuniro cha Iye amene anandituma Ine ndi ichi, kuti yense wakuwona Mwana, ndi kukhulupirira pa Iye, akhale nawo moyo wosatha: ndipo Ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomaliza. Yohane 6:40
“Koma kwa ife kuli Mulungu mmodzi, Atate, amene zinthu zonse zichokera kwa Iye, ndi ife mwa Iye; ndi Ambuye mmodzi Yesu Khristu, amene mwa Iye muli zinthu zonse, ndi ife mwa Iye.”—1 Akorinto 8:6.
“Pakuti pali Mulungu mmodzi, ndi mkhalapakati mmodzi pakati pa Mulungu ndi anthu, munthu Khristu Yesu.” 1 Timoteo 2:5
“Chisomo chikhale ndi inu, ndi mtendere wochokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Khristu. 1 Akorinto 1:3
“Taonani mtumiki wanga amene ndamusankha, wokondedwa wanga, amene moyo wanga ukondwera naye. Mateyu 12:18
“Musadzipangire nokha fano losema, kapena chifaniziro chirichonse cha zinthu za m’thambo la kumwamba, kapena za m’dziko lapansi, kapena za m’madzi a pansi pa dziko; iwo.” Deuteronomo 5:8, 9
“(iwo) anasandutsa ulemerero wa Mulungu wosawonongeka, naupanga chifaniziro cha munthu wowonongeka, ndi mbalame, ndi nyama za miyendo inayi, ndi zokwawa.” Aroma 1:23
“Tiana, dzisungireni nokha kwa mafano; Yohane 5:21
“Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha. Yohane 3:16
“Ndipo palibe chipulumutso mwa wina aliyense, pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo la kumwamba, lopatsidwa mwa anthu, limene tiyenera kupulumutsidwa nalo. Machitidwe 4:12
“Ine ndine khomo; ngati munthu alowa ndi Ine, adzapulumutsidwa, nadzalowa, nadzatuluka, nadzapeza msipu. Yohane 10:9
“Yesu anayankha kuti, ‘Ine ndine njira, choonadi ndi moyo. Palibe amene amafika kwa Atate osadzera mwa ine.’”— Yohane 14:6
We are all invited by God to reason together with Him. This attitude of God toward man is an expression of His Love. God has given us His Word, the Bible, where we find answers to all of life’s important questions. Therefore, let us turn to this Wonderful Book for the answers to some vital questions which most of us, at some time or another, have pondered. The texts quoted herein were selected with due consideration to the context which is the only honest way to find accurate Scriptural answers. The questions on the following pages are among the most important that present themselves to our minds and are fully answered in the Bible. These are only samples of many more Scriptural citations that could be given. Jesus said, “If you continue In my word, then are you my disciples indeed; you shall know the truth, and the truth shall make you free." John 8:31-32
“Which in His times He shall show who is the blessed and only Potentate, the King of Kings, and Lord of lords, who only has immortality, dwelling in the Light which no man can approach unto, whom no man has seen, nor can see!” 1 Timothy 6:15, 16
"The soul that sins, it shall die." Ezekiel 18:20
"Fear not them which kill the body but are not able to kill the soul; but rather fear Him who is able to destroy both soul and body in Gehenna.” Matthew 10:28
"In the sweat of thy face shall you eat bread, till you return to the ground; for out of it were you taken: dust you are, and to dust shall you return.” (Referring to death of the body.) Genesis 3:19
"But I would not have you to be ignorant, brethren, concerning those which are asleep (dead) that you sorrow not, even as others which have no hope.” 1 Thessalonians 4:13
"His breath goes forth, he returns to his earth; in that very day his thoughts perish.” Psalm 146:4
"... no man has ascended up to heaven, except He that came down from heaven, even the Son of Man.” (All are still in their graves until the resurrection.) John 3:13
"...if the dead rise not, then Christ is not raised; and if Christ is not raised, your faith is vain; you are yet In your sins. Then they also which are asleep in Christ are perished.” 1 Corinthians 15:15-18
"For the Lord Himself shall descend from heaven with a shout, with the voice of the Archangel, and the trump of God; and the dead in Christ shall rise first." 1 Thessalonians 4:16
"For as in Adam all die, even so in Christ shall all be made alive.” 1 Corinthians 15:21, 22
"...the hour is coming when all that are in the graves shall hear His voice, and shall come forth.” John 5:28, 29
"...this is the will of Him that sent me, that every one which sees the Son, and believes on Him, may have everlasting life: and I will raise him up at the last day.” John 6:40
"But to us there is but one God, the Father, of whom are all things, and we in Him; and one Lord Jesus Christ by whom are all things, and we by Him” 1 Corinthians 8:6
“For there is one God and one mediator between God and men, the man Christ Jesus." 1 Timothy 2:5
"Grace be unto you and peace from God our Father, and from the Lord Jesus Christ." 1 Corinthians 1:3
"Behold my servant, whom I have chosen; my beloved, in whom my soul is well pleased. I will put my spirit upon Him and He shall show judgment to the Gentiles." Matthew 12:18
"You shall not make unto yourselves any graven image, or any likeness of anything that is in heaven above, or that is in the earth beneath, or that is in the waters beneath the earth: You shall not bow down yourselves unto them nor serve them.” Deuteronomy 5:8, 9
“(they) changed the glory of the incorruptible God Into an image made like to corruptible man, and to birds, and four-footed beasts, and things which creep." Romans 1:23
"Little children, keep yourselves from idols." John 5:21
"God so loved the world, that he gave His only begotten Son, that whoever believes in Him should not perish but have everlasting life." John 3:16
"Neither is there salvation in any other, for there is no other name under heaven given among men, whereby we must be saved." Acts 4:12
“I am the door: by me if any man enter in, he shall be saved, and shall go in and out, and find pasture.” John 10:9
“Jesus answered, ‘I am the way and the truth and the life. No one comes to the Father except through me.’” John 14:6
Kodi Gahena Ndi Chiyani (Gawo 1)
Kuphunzira Baibulo —Chitsogozo
Just What Is Hell (Part 1)
Studying The Bible - A Guide