Ndife okondwa kwambiri kuti muli pano, ndipo tikupemphera kuti mupeze chinachake pano chimene chidzakhala dalitso lalikulu kwa inu ngati mukufuna kukhala Mkristu wamphamvu ndi waufulu kuposa momwe mukuganizira lero.
Tiyembekezela mwacidwi kuona mmene tingakuthandizireni kukula ndi kukhwima mwa Khristu, kuti mukhale ndi moyo pamaso pa Mulungu monga mmene mumafunira, ndi kupezeka kuti mum’kondweretsa. Ichi ndi cholinga chaumwini cha aliyense amene amagwira ntchito mongodzipereka m’gululi, ndipo tikufuna kugawana nanu zinthu zimene zatidalitsa. Tikuyembekezera kuti inunso mugawane nafe, zinthu zomwe zakudalitsani inu.
Buku la Genesis limatiuza kuti ngakhale Adamu ndi Hava anali maliseche m’munda wa Edeni, sanachite manyazi (Genesis 2:25). Koma taonani zimene zinachitika atangodya chipatso choletsedwacho. "Ndiye...